spot_img
Saturday, February 1, 2025
spot_img
HomeLatestUsi wati a Malawi ali ndi mtima wa "Khwizi"

Usi wati a Malawi ali ndi mtima wa “Khwizi”

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Michael Usi, wati m’dziko muno muli anthu oyipa amene amafuna anzawo adzidutsa muzovuta nthawi zonse.

Dr Usi ati pali anthu ena amene akaona mmera wabwino m’munda sakukondwa kaamba koti akufuna anthu m’dziko muno akhale ndi njala ndikumavutika.

“Ena, mafuta agalimoto omwewa, akufuna adzisowa cholinga adzisangalala ndi kuvutika kwa anthu akakhala pa nzere kufuna mafutawa,” atero Dr Usi.

Wachiwiri kwa mtsogoleriyu anena izi pomwe ali nawo pa mwambo okhazikitsa ntchito yolalikila anthu ya chaka chino pa mpingo wa Zomba Central Seventh Day.

Iwo awarenga mau a Baibulo ochokera pa Mateyu 28 vesi 18 mpaka 20 pomwe akukamba zokalalikira kwa anthu kuti apulumutsidwe ku machimo.

A Ernest Kaonga, omwe ndi otsogolera ntchito yaulaliki mu mpingowu, ndiwo alalikira pa tsikuli.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular