spot_img
Saturday, February 1, 2025
spot_img
HomeLatestAmumanga Atapisa Mmaso Oweluza Milandu

Amumanga Atapisa Mmaso Oweluza Milandu

Damiano Nkhoma, wazaka 42, alimanja mwa Polisi ya Lilongwe atabera Majisitireti wina ndalama zokwana K400, 000 mwaukatyali.

Malingana ndi mneneri wa Police ya Lilongwe Hastings Chigalu, Nkhoma ananamiza nkulu wa khoti yu kuti amapedzera anthu nyumba za renti, ndipo panthawiyo adanama kuti ali ndi ina imodzi.

Chigalu wati, Nkhoma anakwanitsa kunamiza Oweluzayu kuti amutumizire ndalama za renti, ina ya malipiro ake apadera komanso ina yoti apangire madongosolo onse oti nyumbai ikhale mmanja mwa Oweluzayu.

Koma mphuno salota, Mkuku Oweluzayu pamodzi ndi banja lake, anagwidwa njakata atafika munzinda wa Lilongwe n’kuzindikira kuti wagwilitsidwa mphepo kamba koti nyumbayo padalibepo.

Ndipo a Chigalu ati oganizilidwayu atafunsidwa, anavomera kuti anachita izi pomwe ankadziwa ndithu kuti mkuku akumubelayo anali Majisitireti.

Nkhoma akuyembekezera kufika ku bwalo la milandu sabata ya mmawa kuti akayankhe mulandu okuba.

RELATED ARTICLES

1 COMMENT

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular