
M’neneri wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) a Jesse Kabwila akuti zinthu zakwera kwambiri m’dziko muno chifukwa cha Democratic Progressive Party (DPP).
Iwo akuti chipani cha DPP chikumatuma anthu kuti azikweza mitengo ya katundu m’dziko muno pofuna kuyipitsa mbiri ya Kongolesi pamodzi ndi m’tsogoleri wawo Chakwera.
A Kabwira akuti pofuna kukonza vuto limeneli Chakwera wasankha a Vitumbiko Mumba ngati nduna ya za malonda kuti athane ndi zimenezi.
Aka sikoyamba akuluakulu achipani cha MCP kunena kuti mavuto omwe ali m’dziko muno ndi chifukwa cha DPP. Mu zaka zinayi zonsezi akhala akunena kuti mavuto onse akupangitsa ndi a DPP.
Kulakhura kwa Jesse Kabwira kukudza ngakhale ma Bishop a katolika adzudzula mchitidwe wosakhala bwino wa a andale omwe akalephera kuyendetsa dziko, akalephera kuthana ndi mavuto amawuza anthu kuti zimenezo zikuchitika chifukwa cha boma lakale zomwe zili zolakwika.