
Mtsogoleli wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera wanenetsa kuti sachoka m’boma kudzera pa zisankho za pa 16 September.
Dr. Chakwera ati salola kuti anthu omwe amaba ndalama ku Reserve Bank komanso ku nyumba zaboma kuti abwelelenso m’boma.
Iwo anena izi pomwe amatsekukira msonkhano wa masiku awiri wa aluso la ntchito zamanja (2025 National Tevet Conference).
Dr. Chakwera ati pakadali pano iwo atseka makomo onse omwe anthu amabera ndalama zaboma.
Mtsogoleli-yu watsindika kuti kutsekaku kuthandiza kuti ndalama zomwe zimabedwa zigwire ntchito yomangira sukulu, misewu ndi zina. (TWR)